Title | : | CRUISE 5 WITH PROFESSOR YUSUF JUWAYEYI - ARCHEOLOGIST |
Duration | : | 48:07 |
Viewed | : | 7,233 |
Published | : | 03-08-2021 |
Source | : | Youtube |
Professor Yusuf Juwayeyi akugwila ntchito ku America ku Long Island University, Brooklyn komwe adayamba ntchito mu 2002.
A Juwayeyi ndi katswiri ofufuza za mbiri ya anthu ndi nyama, pachingelezi Archeologist. Iwo afufuza zambiri mdziko la Malawi komanso kunja – ntchito yomwe imakhudza kukumba pansi kuti apeze mafupa aanthu ndi nyama zakalekale, komanso ziwiya zawo kuti amvetse mmene zinthu zinkakhalira kalelo.
Pano a Juwayeyi alemba buku lotchedwa Archaeology and Oral Tradition in Malawi: Origins and Early History of the Chewa. Bukuli likukamba za mbiri ya aChewa, kumene adachokera, kumene adafikila kuno ku Malawi komanso makhalidwe awo amakedzana. Iwo akuti adafukula mafupa a aChewa amene adakhala ku Mankhamba. Akuti adapeza umboni wakuti aChewa anthawiyo anali achuma kwambiri ndi zina zopatsa chidwi zomwe alemba mu bukuli.
Professor Yusuf Juwayeyi adabadwa ndikukulira ku Malawi. Aphunzitsako ku Chancellor College, Hunter College ya City University yaku New York komanso ngati oyesa mayeso a Archaeology ku University of Dar-es-Salaam ku Tanzania mu 1993.
Anagwilako mboma ku Malawi ku Department of Antiquities mu 1989 kenako ngati Commissioner for Culture mu 1992. Mchaka cha 2000 anasankhidwa kukakhala kazembe wadziko la Malawi ku United Nations ku New York.
SHARE TO YOUR FRIENDS
Scan me